Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.
Mateyu 8:19 - Buku Lopatulika Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kulikonse mumukako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kulikonse mumukako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma nthaŵi yomweyo padafika mphunzitsi wina wa Malamulo namuuza kuti, “Aphunzitsi, ndizikutsatani kulikonse kumene muzipita.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mphunzitsi wa malamulo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ine ndidzakutsatani kulikonse kumene muzipita.” |
Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.
Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sangathe kukhala wophunzira wanga.
Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitse nzeru ya dziko lapansi?
ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yachisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako.