Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 7:3 - Buku Lopatulika

Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako?

Onani mutuwo



Mateyu 7:3
10 Mawu Ofanana  

Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli.


Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.


Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;


Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.


Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.