Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu, chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.
Mateyu 7:28 - Buku Lopatulika Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atatsiriza kunena zimenezi, anthu onse aja adadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atamaliza kunena zonsezi, magulu a anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, |
Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu, chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.
Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ake khumi ndi awiri, Iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m'mizinda mwao.
Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anachokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordani.
ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.
Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.
Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
Ndipo pofika tsiku la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake?
Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?