Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Mateyu 7:24 - Buku Lopatulika Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. |
Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.
Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.
Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.
Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?
Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.
ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwe; chifukwa inakhazikika pathanthwepo.
Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga;
Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.
pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama.