Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.
Mateyu 7:20 - Buku Lopatulika Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho mudzaŵadziŵira zochita zao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Momwemonso, ndi zipatso zawo iwo mudzawazindikira. |
Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.
Pakuti mtengo uliwonse uzindikirika ndi chipatso chake. Pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa.
Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka;
Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.