Mateyu 6:21 - Buku Lopatulika pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko. |
Ndipo kudzakhala chilimbiko m'nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake.
Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.
Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?
Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.
Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako lili la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa.
Ulibe gawo kapena cholandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.
popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.
ine Paulo ndichilemba ndi dzanja langa, ndidzachibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga.
Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;