Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.
Mateyu 6:17 - Buku Lopatulika Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m'maso nkudzola mafuta kumutu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu, |
Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.
Ndipo Yowabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nuvale zovala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikulu.
Usambe tsono, nudzole, nuvale zovala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.