Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake; ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.
Mateyu 6:11 - Buku Lopatulika Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutipatse ife lero chakudya chathu chamasikuwonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mutipatse chakudya chathu chalero. |
Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake; ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.
Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;
iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.
Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.
Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha.
Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m'dziko la Mowabu; pakuti adamva m'dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.