Mateyu 5:47 - Buku Lopatulika Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okha, mwachitapo chiyani pamenepo choposa ena? Kodi suja ngakhale akunja amachita chimodzimodzi? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ngati inu mupatsa moni abale anu okhaokha mukuchita chiyani choposa ena? Kodi ngakhale akunja sachita chimodzimodzi? |
Pakuti ndinena ndi inu, ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.
Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?
Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti ochimwa omwe akonda iwo akukondana nao.
Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu.