Mateyu 5:43 - Buku Lopatulika Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Ukonde mnzako, ndi kudana ndi mdani wako.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Munamva kuti, ‘Konda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako.’ |
Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.
Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu:
Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;
Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino:
Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.