Mateyu 5:42 - Buku Lopatulika Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize. |
Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.
Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.
Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a moto pamutu pake.
Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.