koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.
Mateyu 5:40 - Buku Lopatulika Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu akakuzenga mlandu nafuna kukulanda mkanjo wako, umlole atengenso ndi mwinjiro wako womwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ngati wina afuna kukuzenga mlandu kuti akulande malaya ako, umupatsenso mkanjo wako. |
koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.
Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya ako.
Koma pamenepo pali chosowa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?
Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe.