Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.
Mateyu 5:31 - Buku Lopatulika Kunanenedwanso, Yense wakuchotsa mkazi wake ampatse iye kalata yachilekaniro: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kunanenedwanso, Yense wakuchotsa mkazi wake ampatse iye chilekaniro: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Anthu akale aja adaaŵalamulanso kuti, ‘Ngati munthu asudzula mkazi wake, ampatse mkaziyo kalata yachisudzulo.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ananena kuti, ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenera amupatse kalata ya chisudzulo.’ |
Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.
Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israele, ndi iye wakukuta chovala chake ndi chiwawa, ati Yehova wa makamu; chifukwa chake sungani mzimu wanu kuti musachite mosakhulupirika.
Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chilichonse?
Iwo ananena kwa Iye, Nanga chifukwa ninji Mose analamula kupatsa kalata yachilekaniro, ndi kumchotsa?