Mateyu 5:29 - Buku Lopatulika Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m'Gehena. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati diso lako la ku dzanja lamanja likuchimwitsa, likolowole nkulitaya. Ndi bwino koposa kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kusiyana nkuti thupi lako lonse aliponye ku Gehena. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati diso lako lakumanja likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. |
Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.
Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire.
Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa Gehena woposa inu kawiri.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.
Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.
Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.
podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo;
pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo.
koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.
Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;