Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 5:17 - Buku Lopatulika

Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadze kupasula, koma kukwaniritsa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Musaganize kuti ndinadza kudzathetsa malamulo kapena zonena za aneneri; sindinabwere kudzathetsa koma kukwaniritsa.

Onani mutuwo



Mateyu 5:17
16 Mawu Ofanana  

Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza.


Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.


Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.


Kuti thambo ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang'ono kachilamulo kagwe nkwapatali.


Koma m'chilamulo Mose anatilamula, tiwaponye miyala otere. Chifukwa chake Inu munena chiyani za iye?


kuti, Uyu akopa anthu apembedze Mulungu pokana chilamulo.


nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao mu Kachisi, nadetsa malo ano oyera.


naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi chilamulo;


Pakuti Khristu ali chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa aliyense amene akhulupirira.


Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo.


kuti choikika chake cha chilamulo chikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.