Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.
Mateyu 4:20 - Buku Lopatulika Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye. |
Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.
Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.
Pomwepo Petro anayankha, nati kwa Iye, onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?
Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedeo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.
kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsane ndi thupi ndi mwazi: