Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa lililonse.
Mateyu 28:7 - Buku Lopatulika Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pitani msanga tsono, kauzeni ophunzira ake aja kuti, ‘Iye wauka kwa akufa, ndipo watsogolako kupita ku Galileya, mukamuwonera kumeneko.’ Kumbukirani zimene ndakuuzanizi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo pitani msanga kawuzeni ophunzira ake kuti, ‘Wauka kwa akufa ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona Iye kumeneko.’ Taonani ndakuwuzani.” |
Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa lililonse.
Nenani inu, tulutsani mlandu wanu; inde, achite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ichi chiyambire nthawi yakale? Ndani wanena ichi kale? Kodi si ndine Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.
Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.
Ndipo iwo anachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukauza ophunzira ake.
Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanene kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.
pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;