Mateyu 28:4 - Buku Lopatulika ndipo ndi kuopsa kwake alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo ndi kuopsa kwake alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo alonda aja adachita mantha nayamba kunjenjemera, nkungoti gwa ngati anthu akufa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alondawo anachita naye mantha kwambiri kotero kuti ananjenjemera ndi kuwuma ngati akufa. |
Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala.
Ndipo pamene iwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitidwa.
Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa.
Ndipo mdindo anaitanitsa nyali, natumphira m'kati, alinkunthunthumira ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Silasi,
Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,