Mateyu 28:16 - Buku Lopatulika Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira khumi ndi mmodzi aja adapita ku Galileya kuphiri kumene Yesu adaapangana nawo kuti akakumane. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ophunzira khumi ndi mmodzi aja anapita ku Galileya, ku phiri limene Yesu anawawuza kuti apite. |
Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.
Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.
amene anamtsata Iye, pamene anali mu Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.
Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.
Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.
Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi?
Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tinachita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Khristu; amene sanamuukitse, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa.