Mateyu 28:12 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akulu, anakhala upo, napatsa asilikaliwo ndalama zambiri, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akulu, anakhala upo, napatsa asilikaliwo ndalama zambiri, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono akulu a ansembe aja ndi akulu a Ayuda adasonkhana napangana nzeru. Adapatsa alonda aja ndalama zambiri, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akulu a ansembe atakumana ndi akuluakulu anapangana zochita. Anapatsa alonda aja ndalama zambiri, |
Ndipo pamene iwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitidwa.
nati, Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo.
Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.
Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.