Mateyu 28:10 - Buku Lopatulika Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yesu adaŵauza kuti, “Musaope. Pitani, kauzeni abale anga kuti apite ku Galileya. Akandiwonera kumeneko.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Musachite mantha, pitani kawuzeni abale anga kuti apite ku Galileya ndipo kumeneko akandiona Ine.” |
Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundichitira ichi Ine.
Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira.
Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa.
Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.
Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, namgwadira.
Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.
Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;
Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.