Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso.
Mateyu 27:60 - Buku Lopatulika nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakauika m'manda ake atsopano ochita chosema m'thanthwe. Tsono adagubuduzira chimwala pa khomo kuti atseke pamandapo, nachoka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anawuyika mʼmanda ake atsopano amene anasema mu thanthwe, natsekapo ndi mwala waukulu pa khomo la mandawo nachokapo. |
Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso.
Uchitanji iwe kuno, ndimo ndani ali nawe kuno, kuti iwe wagoba manda kuno, ndi kudzigobera manda pamwamba, ndi kudzisemera mogonamo m'thanthwe.
Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m'kamwa mwake munalibe chinyengo.
Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.
Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.
Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa Iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.
Pomwepo anachotsa mwala. Koma Yesu anakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.
Koma kunali munda kumalo kumene anapachikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwemo munthu aliyense nthawi zonse.
Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.