Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.
Mateyu 27:47 - Buku Lopatulika Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamene anamva, ananena, Uyo aitana Eliya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamene anamva, ananena, Uyo aitana Eliya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamva mauwo, ena amene adaaimirira pamenepo adati, “Munthuyu akuitana Eliya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ena a oyimirira pamalopo atamva izi anati, “Akuyitana Eliya.” |
Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.
Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?
Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, natenga chinkhupule, nachidzaza ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye.