Ndipo pakutsimphina ine anakondwera, nasonkhana pamodzi; akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinachidziwe, ananding'amba osaleka.
Mateyu 27:44 - Buku Lopatulika Ndiponso achifwambawo opachikidwa pamodzi ndi Iye, anamlalatira Iye mau amodzimodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso achifwambawo opachikidwa pamodzi ndi Iye, anamlalatira Iye mau amodzimodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zigaŵenga zimene adaazipachika pamodzi ndi Yesu zija, nazonso zinkamunyoza chimodzimodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Momwemonso mbala zimene zinapachikidwa naye pamodzi zinamuneneranso zachipongwe. |
Ndipo pakutsimphina ine anakondwera, nasonkhana pamodzi; akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinachidziwe, ananding'amba osaleka.
Pamenepo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri, mmodzi kudzanja lamanja, ndi wina kulamanzere.
Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.
Pakuti Khristunso sanadzikondweretse yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa Ine.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.