nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.
Mateyu 27:42 - Buku Lopatulika Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye mwini. Si Mfumu ya Aisraele nanga? Atsiketu tsopano pamtandapo kuti timkhulupirire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anati, “Anapulumutsa ena koma sangathe kudzipulumutsa yekha! Ndi mfumu ya Israeli! Mulekeni atsike pa mtanda ndipo tidzamukhulupirira Iye. |
nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.
nati, Nanga Iwe, wopasula Kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.
Moteronso ansembe aakulu anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sangathe kudzipulumutsa yekha.
Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.
nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere mu Mwamba, ndi ulemerero mu Mwambamwamba.
Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.
anatenga makwata a kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye mfumu ya Israele.
Ndipo ngati wina akumva mau anga, ndi kusawasunga, Ine sindimweruza; pakuti sindinadze kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi.
Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.
Ndipotu pakuona munthu wochiritsidwayo alikuimirira pamodzi nao, analibe kanthu kakunena kotsutsa.