Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.
Mateyu 27:34 - Buku Lopatulika anamwetsa Iye vinyo wosakaniza ndi ndulu; ndipo Iye, m'mene analawa, sanafune kumwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 anamwetsa Iye vinyo wosanganiza ndi ndulu; ndipo Iye, m'mene analawa, sanafune kumwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumeneko adapatsa Yesu vinyo wosanganiza ndi ndulu kuti amwe. Koma atalaŵa, adakana kumwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo anamupatsa vinyo wosakaniza ndi ndulu kuti amwe; koma atalawa anakana kumwa. |
Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.
Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'mizinda yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.
Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, natenga chinkhupule, nachidzaza ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye.
Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,