Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.
Mateyu 27:26 - Buku Lopatulika Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Pilato adaŵamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo anawamasulira Baraba koma analamula kuti Yesu akakwapulidwe, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe. |
Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.
Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.
nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.
ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.
Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda.
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.