Mateyu 27:23 - Buku Lopatulika Ndipo iye anati, Chifukwa ninji? Anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsa kopambana, Apachikidwe pamtanda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anati, Chifukwa ninji? Anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsa kopambana, Apachikidwe pamtanda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pilato adaŵafunsanso kuti, “Adalakwanji?” Koma anthu aja adafuula koposa kuti, “Apachikidwe pa mtanda!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wachita choyipa chotani?” Koma anachita phokoso nafuwula kwambiri kuti, “Mpachikeni!” |
Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda.
Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.
Ndipo Pilato anati kwa ansembe aakulu ndi makamu a anthu, Ndilibe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu.
Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.