Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali; munandiika ndiwakhalire chonyansa. Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.
Mateyu 27:21 - Buku Lopatulika Koma kazembe anati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo anati, Barabasi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma kazembe anati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo anati, Barabasi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono bwanamkubwa uja adaŵafunsa kuti, “Mukufuna kuti ndikumasulireni uti mwa aŵiriŵa?” Anthu aja adati, “Barabasi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Bwanamkubwayo anafunsa kuti, “Ndi ndani mwa awiriwa amene mufuna ine ndikumasulireni?” Iwo anayankha kuti, “Baraba.” |
Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali; munandiika ndiwakhalire chonyansa. Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.
Chifukwa chake pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Barabasi kodi, kapena Yesu, wotchedwa Khristu?
Koma ansembe aakulu ndi akulu anapangira anthu kuti apemphe Barabasi, koma kuti aononge Yesu.
Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda.
Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzake, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu.