Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.
Mateyu 27:12 - Buku Lopatulika Ndipo pakumnenera Iye ansembe aakulu ndi akulu, Iye sanayankhe kanthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakumnenera Iye ansembe aakulu ndi akulu, Iye sanayankhe kanthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma pamene akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda aja ankamuneneza, Yesu sadayankhepo kanthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene akulu a ansembe ndi akuluakulu ankamuneneza, sanayankhe kanthu. |
Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.
Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.
Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo: Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga, kotero sanatsegule pakamwa pake.
amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;