Ndipo ndinanena nao, Chikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwake masekeli a siliva makumi atatu.
Mateyu 27:10 - Buku Lopatulika ndipo anazipereka kugula munda wa woumba mbiya, monga anandilamulira ine Ambuye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anazipereka kugula munda wa woumba mbiya, monga anandilamulira ine Ambuye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa nagulira munda wa mmisiri wa mbiya, monga momwe Ambuye adaandilamulira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anazigwiritsa ntchito kugula munda wa wowumba mbiya monga mmene Ambuye anandilamulira ine.” |
Ndipo ndinanena nao, Chikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwake masekeli a siliva makumi atatu.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wake wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga masekeli makumi atatu a siliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m'nyumba ya Yehova.