Mateyu 26:68 - Buku Lopatulika nati, Utilote ife, Khristu Iwe; wakumenya Iwe ndani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nati, Utilote ife, Khristu Iwe; wakumenya Iwe ndani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa nkumanena kuti, “Iwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, nanga sindiwe mneneri? Lota, wakumenya ndani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anati, “Tanenera kwa ife, Khristu. Wakumenya ndani?” |
Ndipo ena anayamba kumthira malovu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo anampanda Iye khofu.
Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samisoni, atisewerere. Naitana Samisoni m'kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuka iye pakati pa mizati.