Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa, chifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zachiwawa.
Mateyu 26:60 - Buku Lopatulika koma sanaupeze zingakhale mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pake anadza awiri, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma sanaupeze zingakhale mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pake anadza awiri, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma sadaupeze ngakhale padaabwera mboni zambiri zabodza. Potsiriza padabwera anthu aŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma sanathe kupeza uliwonse, angakhale kuti mboni zambiri zabodza zinapezeka. Pomalizira mboni ziwiri zinabwera patsogolo. |
Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa, chifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zachiwawa.
Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iliyonse, kapena tchimo lililonse adalichimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.
mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.
ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.