Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi chimenechi ndi chifundo chako cha pa bwenzi lako? Unalekeranji kupita ndi bwenzi lako?
Mateyu 26:50 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamuuza kuti, “Bwenzi langa, chita zimene wadzera.” Apo anthu aja adabwera namugwira Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Bwenzi langa, chita chimene wabwerera.” Pamenepo anthuwo anabwera patsogolo namugwira Yesu ndi kumumanga. |
Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi chimenechi ndi chifundo chako cha pa bwenzi lako? Unalekeranji kupita ndi bwenzi lako?
Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.
Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangane ndi ine pa rupiya latheka limodzi?
nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala nacho chovala cha ukwati? Ndipo iye analibe mau.