Mateyu 26:49 - Buku Lopatulika Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yudasi adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti, “Moni Aphunzitsi!” Atatero adamumpsompsona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Yudasi anapita kwa Yesu nati, “Moni, Aphunzitsi!” Ndipo anapsompsona Iye. |
Ndipo Yowabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuti ampsompsone.
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Ndipo Yudasi, womperekayo anayankha nati, Kodi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.
Koma wompereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye.
Sunandipatsa mpsompsono wa chibwenzi; koma uyu sanaleke kupsompsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine.
Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?