Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Iskariote, anamuka kwa ansembe aakulu,
Mateyu 26:47 - Buku Lopatulika Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu akulankhula choncho, wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akuyankhula choncho, Yudasi mmodzi mwa khumi ndi awiriwo anafika. Pamodzi ndi iye panali gulu lalikulu la anthu ali ndi mikondo ndi zibonga otumidwa ndi akulu a ansembe ndi akuluakulu. |
Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Iskariote, anamuka kwa ansembe aakulu,
Koma wompereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye.
Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.
Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.