Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja, pena wogona pansonga ya mlongoti wa ngalawa.
Mateyu 26:43 - Buku Lopatulika Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atabweranso anawapeza ali mtulo chifukwa zikope zawo zinalemedwa ndi tulo. |
Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja, pena wogona pansonga ya mlongoti wa ngalawa.
Ndipo mwini chombo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? Uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukira tingatayike.
Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe.
Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye.
Ndipo mnyamata dzina lake Yutiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anamtola wakufa.
Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.