Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.
Mateyu 26:42 - Buku Lopatulika Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adachokanso kachiŵiri nakapemphera kuti, “Atate, ngati chikho chamasautsochi sichingandichoke, mpaka nditamwa ndithu, chabwino, zimene mukufuna zichitike.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti, “Atate anga, ngati chikhochi sichingandichoke, mpaka nditamwa, kufuna kwanu kuchitike.” |
Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.
Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.
Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu.
nati, Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kuchitike.
Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.
Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.