Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.
Mateyu 26:36 - Buku Lopatulika Pomwepo Yesu anadza ndi iwo kumalo otchedwa Getsemani, nanena kwa ophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Yesu anadza ndi iwo kumalo otchedwa Getsemani, nanena kwa ophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti, “Inu bakhalani pano, Ine ndikupita uko kukapemphera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti, “Khalani pano pamene Ine ndikukapemphera apo.” |
Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.
Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe.
Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,