Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,
Mateyu 26:30 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atayimba nyimbo, anatuluka kupita ku phiri la Olivi. |
Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,
Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi champesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga.
Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa mu Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona paphiri lotchedwa la Azitona.
Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye.
koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndi kuti ndichita monga momwe Atate wandilamula. Nyamukani, tizimuka kuchokera kuno.