Mateyu 26:27 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anatenga chikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ichi inu nonse, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anatenga chikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ichi inu nonse, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo nati, “Imwani nonsenu. |
Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi: Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga; ndadya uchi wanga ndi chisa chake; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi.
M'kamwa mwako munge ngati vinyo woposa, womeza tseketseke bwenzi langa, wolankhulitsa milomo ya ogona tulo.
Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.
Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake.
natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.
Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa.
pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.
Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.
Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?