Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.
Mateyu 26:26 - Buku Lopatulika Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, idyani, ili ndi thupi langa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, idyani; ili ndi thupi langa.” |
Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.
Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo.
Ndipo analandira chikho, ndipo pamene adayamika, anati, Landirani ichi, muchigawane mwa inu nokha;
Ndipo kunali m'mene Iye anaseama nao pachakudya, anatenga mkate, naudalitsa, naunyema, napatsa iwo.
Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.
namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu.