Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse?
Mateyu 26:25 - Buku Lopatulika Ndipo Yudasi, womperekayo anayankha nati, Kodi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yudasi, womperekayo anayankha nati, Kodi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yudasi, amene pambuyo pake adapereka Yesu, adafunsa kuti, “Monga nkukhala ine, Aphunzitsi?” Yesu adamuyankha kuti, “Wanena wekha.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yudasi amene anamupereka Iye anati, “Monga nʼkukhala ine Aphunzitsi?” Yesu anayankha nati, “Iwe watero.” |
Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse?
Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachite zoipa.
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Iskariote, anamuka kwa ansembe aakulu,
Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.
Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.
Ndipo onse anati, Umo mtero, muli Mwana wa Mulungu kodi? Ndipo Iye anati kwa iwo, Munena kuti ndine.
Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga.