Mateyu 26:19 - Buku Lopatulika Ndipo ophunzira anachita monga Yesu anawauza, nakonza Paska. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ophunzira anachita monga Yesu anawauza, nakonza Paska. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira aja adapita nakachita zomwe Yesu adaaŵauza, nakakonzadi za phwando la Paska. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo ophunzira ake anachita monga momwe Yesu anawawuzira ndipo anakonza Paska. |
Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wina wake, mukati kwa Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.
Ndipo pakufika madzulo, Iye analinkukhala pachakudya pamodzi ndi ophunzira khumi ndi awiri;