Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.
Mateyu 26:17 - Buku Lopatulika Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paska, kuti mukadye? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paska, kuti mukadye? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, ophunzira aja adadza nafunsa Yesu kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku loyamba laphwando la buledi wopanda yisiti, ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonze kuti malo odyera Paska?” |
Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.
Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.