nati, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.
Mateyu 26:16 - Buku Lopatulika Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono kuyambira pomwepo iye adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuyambira pamenepo Yudasi anafunafuna nthawi yabwino yoti amupereke Yesu. |
nati, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.
Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paska, kuti mukadye?
Ndipo pamene iwo anamva, anasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye anafunafuna pompereka Iye bwino.
Ndipo iye anavomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.
Ndipo m'mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.
Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi.