Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma.
Mateyu 26:10 - Buku Lopatulika Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu podziŵa zimene iwo aja ankalankhula, adaŵafunsa kuti, “Mukumuvutiranji maiyu? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu podziwa izi anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino. |
Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma.
M'mene Iye anali chilankhulire, anadza wina wochokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usamvute Mphunzitsi.
Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;
Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu.
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;
Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna ntchito yabwino.
wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.
Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.
Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;
Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.
Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a ntchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;
akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.