Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda: Ndinamfunafuna, koma osampeza.
Mateyu 25:5 - Buku Lopatulika Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Popeza kuti mkwati adaachedwa, onse aja adayamba kuwodzera, nagona tulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mkwati anachedwa ndipo onse anayamba kusinza nagona. |
Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda: Ndinamfunafuna, koma osampeza.
Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso: Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati, nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga, nkhunda yanga, wangwiro wanga. Pakuti pamutu panga padzala mame, patsitsi panga pali madontho a usiku.
Ndinayankha kuti, Ndavula malaya anga, ndiwavalenso bwanji? Ndatsuka mapazi anga; ndiwadetserenji?
Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.
Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m'tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? Simungathe kuchezera ndi Ine mphindi imodzi?
Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;
Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa Munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?
Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wampesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu.
Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: