Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa, chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.
Mateyu 25:4 - Buku Lopatulika koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo. |
Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa, chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe;
Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso.
Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.
Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.