Mateyu 25:3 - Buku Lopatulika Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengerenso mafuta; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta; |
Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ochita chilungamo, osasiya chilangizo cha Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.
Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati.
akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.
ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.